Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 19:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Anthu a mu Iguputo adzadabwa kwambiri+ ndipo ine ndidzasokoneza zolinga za dzikolo.+ Iwo adzafunsira kwa milungu yopanda pake,+ kwa anthu amatsenga, kwa olankhula ndi mizimu ndiponso kwa olosera zam’tsogolo.+

  • Yesaya 47:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Alangizi ako ambirimbiri akutopetsa. Anthu opembedza zinthu zakumwamba, oyang’anitsitsa kayendedwe ka nyenyezi,+ amene amalosera zimene zichitike kwa iwe mwezi watsopano ukakhala, tsopano aimirire ndi kukupulumutsa.

  • Danieli 2:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Akasidiwo anayankha mfumuyo kuti: “Palibe munthu padziko lapansi amene angathe kuuza inu mfumu zimene mukufuna, pakuti palibe mfumu yaikulu kapena bwanamkubwa amene anauzapo wansembe wochita zamatsenga kapena munthu wolankhula ndi mizimu kapena Mkasidi kuti achite zimenezi.

  • Danieli 2:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Chinsinsi chimene inu mfumu mukufuna kudziwa, amuna anzeru, anthu olankhula ndi mizimu, ansembe ochita zamatsenga ndi anthu okhulupirira nyenyezi, alephera kukuuzani.+

  • Danieli 4:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 “Chotero ansembe ochita zamatsenga, anthu olankhula ndi mizimu, Akasidi*+ ndi okhulupirira nyenyezi+ anabwera kwa ine ndipo ndinawauza malotowo, koma iwo sanathe kuwamasulira.+

  • Danieli 5:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ndiyeno mfumuyo inafuula kuti aibweretsere olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi okhulupirira nyenyezi.+ Mfumuyo inauza amuna anzeru a m’Babulo amenewa kuti: “Aliyense amene angawerenge mawuwa ndi kundiuza kumasulira kwake, ndimuveka zovala zofiirira*+ ndi mkanda wagolide m’khosi, ndipo ndimuika kukhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena