Numeri 12:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Iye anawauza kuti: “Mvetserani mawu anga. Pakanakhala mneneri wa Yehova pakati panu, ndikanamudziwitsa za ine m’masomphenya,+ ndipo ndikanalankhula naye m’maloto.+ Yobu 33:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Iye amawalankhula m’maloto+ ndi m’masomphenya+ a usiku,Anthu akakhala m’tulo tofa nato,Akamagona pabedi.+ Salimo 25:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa,+Pangano lakenso ndi la anthu oterowo, ndipo iye amawadziwitsa panganolo.+ Danieli 2:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Koma kuli Mulungu kumwamba amene ndi Woulula zinsinsi,+ ndipo wakudziwitsani, inu Mfumu Nebukadinezara, zimene zidzachitike m’masiku otsiriza.+ Maloto anu ndi masomphenya amene munaona muli pabedi lanu ndi awa: 1 Akorinto 2:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Kodi ndi munthu uti amene angadziwe za munthu kupatulapo mzimu+ umene uli mwa munthuyo? Momwemonso, palibe amene akudziwa zinthu za Mulungu, kupatulapo mzimu+ wa Mulungu.
6 Iye anawauza kuti: “Mvetserani mawu anga. Pakanakhala mneneri wa Yehova pakati panu, ndikanamudziwitsa za ine m’masomphenya,+ ndipo ndikanalankhula naye m’maloto.+
15 Iye amawalankhula m’maloto+ ndi m’masomphenya+ a usiku,Anthu akakhala m’tulo tofa nato,Akamagona pabedi.+
14 Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa,+Pangano lakenso ndi la anthu oterowo, ndipo iye amawadziwitsa panganolo.+
28 Koma kuli Mulungu kumwamba amene ndi Woulula zinsinsi,+ ndipo wakudziwitsani, inu Mfumu Nebukadinezara, zimene zidzachitike m’masiku otsiriza.+ Maloto anu ndi masomphenya amene munaona muli pabedi lanu ndi awa:
11 Kodi ndi munthu uti amene angadziwe za munthu kupatulapo mzimu+ umene uli mwa munthuyo? Momwemonso, palibe amene akudziwa zinthu za Mulungu, kupatulapo mzimu+ wa Mulungu.