Salimo 12:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Iwo amalankhulana zabodza.+Amalankhulana ndi milomo yoshashalika+ komanso ndi mitima iwiri.+ Salimo 58:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Oipa akhala opotoka maganizo kuyambira ali m’mimba.+Iwo asochera kuyambira ali m’mimba,Ndipo amalankhula zabodza.+ Salimo 64:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Amaumirira kulankhula zoipa,+Amakambirana kuti atchere misampha.+Iwo amati: “Angaione ndani?”+ Miyambo 12:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Maganizo a anthu olungama ndiwo chilungamo.+ Utsogoleri wa anthu oipa ndi wachinyengo.+ Miyambo 12:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Chinyengo chimakhala mumtima mwa anthu okonza chiwembu,+ koma olimbikitsa mtendere amasangalala.+ Miyambo 26:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Milomo yonena zabwino mwachiphamaso koma mumtima muli zoipa, ili ngati siliva wokutira phale.+ 1 Timoteyo 4:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Zimenezi zidzachitikanso chifukwa cha chinyengo cha anthu olankhula mabodza,+ amene chikumbumtima chawo chili ngati chipsera+ chobwera chifukwa chopsa ndi chitsulo chamoto.
3 Oipa akhala opotoka maganizo kuyambira ali m’mimba.+Iwo asochera kuyambira ali m’mimba,Ndipo amalankhula zabodza.+
2 Zimenezi zidzachitikanso chifukwa cha chinyengo cha anthu olankhula mabodza,+ amene chikumbumtima chawo chili ngati chipsera+ chobwera chifukwa chopsa ndi chitsulo chamoto.