Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 10:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Iye amaperekera chiweruzo ana amasiye* ndi akazi amasiye,+ ndipo amakonda mlendo wokhala pakati panu+ moti amam’patsa mkate ndi chofunda.

  • Salimo 10:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Inu mwaona mavuto ndi masautso.

      Mumawayang’anabe kuti muchitepo kanthu.+

      Waumphawi,+ mwana wamasiye,* amadziikiza m’manja mwanu.

      Inu mwakhala mthandizi wake.+

  • Salimo 68:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Tate wa ana amasiye* ndi woweruzira akazi amasiye milandu,+

      Ndi Mulungu amene amakhala m’malo ake oyera.+

  • Salimo 146:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Yehova amayang’anira alendo okhala m’dziko la eni.+

      Amathandiza mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye.+

      Koma njira+ ya anthu oipa amaichititsa kukhala yovuta kuyendamo.+

  • Miyambo 23:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pakuti Wowawombola ndi wamphamvu, ndipo adzawateteza pa mlandu wawo ndi iwe.+

  • Yakobo 1:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Kupembedza koyera+ ndi kosaipitsidwa+ kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye+ ndi akazi amasiye+ m’masautso awo,+ ndi kukhala wopanda banga+ la dzikoli.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena