Masalimo
2 Ndidzatamanda Yehova pamene ndili moyo.+
Ndidzaimbira Mulungu wanga nyimbo zomutamanda kwa moyo wanga wonse.+
3 Musamakhulupirire anthu olemekezeka,+
Kapena mwana wa munthu wina aliyense wochokera kufumbi amene alibe chipulumutso.+
4 Mzimu* wake umachoka,+ ndipo iye amabwerera kunthaka.+
Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.+
5 Wodala ndi munthu amene thandizo lake limachokera kwa Mulungu wa Yakobo,+
Amene chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake,+
6 Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi,+
Nyanja ndi zonse zili mmenemo.+
Wosunga choonadi mpaka kalekale.+
7 Iye ndi Woperekera chiweruzo anthu ochitiridwa chinyengo,+
Wopereka chakudya kwa anthu anjala.+
Yehova amamasula anthu omangidwa.+
8 Yehova amatsegula maso a anthu akhungu.+
Yehova amaweramutsa anthu owerama chifukwa cha masautso.+
Yehova amakonda anthu olungama.+