33 Ine ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo ndidzakusololerani lupanga ndi kukupitikitsani.+ Dziko lanu lidzakhala bwinja,+ ndipo mizinda yanu idzawonongedwa ndi kukhala mabwinja.
31 Ine ndidzaimba mlandu Yehoyakimu,+ ana ake ndi atumiki ake chifukwa cha zolakwa zawo.+ Anthu amenewa komanso anthu okhala mu Yerusalemu ndi anthu a mu Yuda ndidzawagwetsera masoka onse amene ndanena.+ Ngakhale kuti ndawauza za masoka onsewa iwo sanamvere.’”’”+