14 Iwo adzauluka paphewa la Afilisiti kumadzulo,+ ndipo onsewa pamodzi, adzalanda katundu wa ana aamuna a Kum’mawa.+ Adzatambasulira dzanja lawo pa Edomu ndi Mowabu,+ ndipo ana a Amoni adzawagonjera.+
19 Iwo adzatenga dera la Negebu kukhala lawo, komanso adzatenga dera lamapiri la Esau,+ dera la Sefela ndi dera la Afilisiti.+ Iwo adzatenganso madera a Efuraimu+ ndi Samariya kukhala awo.+ Benjamini adzatenga dera la Giliyadi+ kukhala lake.