Mateyu 16:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Kuyambira pamenepo, Yesu Khristu anayamba kuuza ophunzira ake kuti n’koyenera kuti iye apite ku Yerusalemu. Kumeneko akazunzidwa kwambiri ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndiyeno akaphedwa, koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.+ Mateyu 20:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Akam’pereka kwa anthu a mitundu ina kuti am’chitire chipongwe, kum’kwapula ndi kum’pachika pamtengo,+ ndipo pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+ Mateyu 27:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Pamenepo anawamasulira Baraba, koma analamula kuti Yesu akwapulidwe+ kenako anamupereka kuti akam’pachike.+ Maliko 15:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Pamenepo Pilato, pofuna kukwaniritsa zofuna za anthuwo,+ anawamasulira Baraba. Ndipo atalamula kuti Yesu amukwapule, anamupereka kuti akamupachike.+ Yohane 19:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Pamenepo anamupereka kwa iwo kuti akamupachike.+ Tsopano Yesu anakhala m’manja mwawo.
21 Kuyambira pamenepo, Yesu Khristu anayamba kuuza ophunzira ake kuti n’koyenera kuti iye apite ku Yerusalemu. Kumeneko akazunzidwa kwambiri ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndiyeno akaphedwa, koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.+
19 Akam’pereka kwa anthu a mitundu ina kuti am’chitire chipongwe, kum’kwapula ndi kum’pachika pamtengo,+ ndipo pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+
26 Pamenepo anawamasulira Baraba, koma analamula kuti Yesu akwapulidwe+ kenako anamupereka kuti akam’pachike.+
15 Pamenepo Pilato, pofuna kukwaniritsa zofuna za anthuwo,+ anawamasulira Baraba. Ndipo atalamula kuti Yesu amukwapule, anamupereka kuti akamupachike.+