12 Pa chifukwa chimenechi, ndidzamupatsa gawo pamodzi ndi ambiri+ ndipo iye adzagawana zolanda ndi amphamvu,+ chifukwa anakhuthula moyo wake mu imfa+ ndipo anaonedwa monga mmodzi wa ochimwa.+ Iye ananyamula tchimo la anthu ambiri+ ndipo analowererapo kuti athandize olakwa.+
31 Kenako, anayamba kuwaphunzitsa kuti Mwana wa munthu ayenera kukumana ndi mavuto ambiri. Iye adzakanidwa ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndiyeno adzaphedwa,+ koma adzauka patapita masiku atatu.+
22 Kenako anati: “Mwana wa munthu ayenera kukumana ndi mavuto ambiri. Iye adzakanidwa ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndiyeno adzaphedwa,+ koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+