Ekisodo 24:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Pamenepo Mose anatenga magaziwo ndi kuwaza anthuwo,+ ndipo anati: “Awa ndiwo magazi okhazikitsira pangano+ limene Yehova wapangana nanu mwa mawu onsewa.” Levitiko 17:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Pakuti moyo wa nyama uli m’magazi+ ndipo ine ndakuikirani magazi paguwa lansembe kuti azikuphimbirani machimo.+ Zili choncho popeza magazi+ ndiwo amaphimba machimo,+ chifukwa moyo uli m’magaziwo. Zekariya 9:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 “Koma mkazi iwe, chifukwa cha magazi a pangano limene unapangana ndi ine,+ ndidzatulutsa akaidi ako+ m’dzenje lopanda madzi. Aheberi 9:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Inde, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi+ malinga ndi Chilamulo, ndipo popanda kukhetsa magazi+ anthu sangakhululukidwe machimo awo.+
8 Pamenepo Mose anatenga magaziwo ndi kuwaza anthuwo,+ ndipo anati: “Awa ndiwo magazi okhazikitsira pangano+ limene Yehova wapangana nanu mwa mawu onsewa.”
11 Pakuti moyo wa nyama uli m’magazi+ ndipo ine ndakuikirani magazi paguwa lansembe kuti azikuphimbirani machimo.+ Zili choncho popeza magazi+ ndiwo amaphimba machimo,+ chifukwa moyo uli m’magaziwo.
11 “Koma mkazi iwe, chifukwa cha magazi a pangano limene unapangana ndi ine,+ ndidzatulutsa akaidi ako+ m’dzenje lopanda madzi.
22 Inde, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi+ malinga ndi Chilamulo, ndipo popanda kukhetsa magazi+ anthu sangakhululukidwe machimo awo.+