Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 ineyo ndidzachotsa Aisiraeli padziko limene ndawapatsa+ ndipo nyumba imene ndaiyeretsa ndi dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Aisiraeli adzawapekera mwambi+ ndi kuwatonza pakati pa mitundu yonse ya anthu.

  • 1 Mafumu 9:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Nyumba iyi idzakhala bwinja.+ Aliyense wodutsa pafupi nayo adzayang’ana modabwa+ ndi kuimba mluzu n’kunena kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova anachita zimenezi padzikoli ndi panyumbayi?’+

  • Yeremiya 7:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 ndidzachita zofanana ndi zimene ndinachita ku Silo.+ Ndidzachita zimenezi panyumba imene ikutchedwa ndi dzina langa,+ imene inu mukuidalira,+ ndiponso malo amene ndinapatsa inu ndi makolo anu.

  • Mika 3:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Chotero Ziyoni adzagawulidwa ngati munda chifukwa cha anthu inu ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.

  • Mateyu 24:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simukuziona zinthu zonsezi? Ndithu ndikukuuzani, Pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa mwala unzake umene sudzagwetsedwa.”+

  • Maliko 13:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Koma Yesu ananena kuti: “Kodi waziona nyumba zapamwamba zimenezi?+ Pano sipadzatsala mwala+ uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.”+

  • Luka 19:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 Iwo adzakuwononga+ limodzi ndi ana ako amene ali mwa iwe. Ndipo sadzasiya mwala pamwala unzake+ mwa iwe, chifukwa sunazindikire kuti nthawi yokuyendera inali itakwana.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena