Yohane 5:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Ndipo Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mwanayo sangachite chilichonse chongoganiza payekha, koma chokhacho chimene waona Atate wake akuchita.+ Pakuti zilizonse zimene Atatewo amachita, Mwana amachitanso zomwezo. Yohane 8:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Pamenepo Yesu anati: “Mukadzamukweza+ Mwana wa munthu,+ pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine amene munali kumuyembekezera uja,+ ndi kutinso sindichita kanthu mongoganiza ndekha.+ Koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.+ Akolose 1:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Iye ndiye chifaniziro+ cha Mulungu wosaonekayo,+ woyamba kubadwa+ wa chilengedwe chonse, Aheberi 1:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Iye amasonyeza ndendende mmene ulemerero wa Mulungu ulili+ ndipo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu weniweniyo,+ ndipo amachirikiza zinthu zonse mwa mawu ake amphamvu.+ Atatiyeretsa potichotsera machimo athu,+ anakhala pansi kudzanja lamanja+ la Wolemekezeka m’malo okwezeka.+
19 Ndipo Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mwanayo sangachite chilichonse chongoganiza payekha, koma chokhacho chimene waona Atate wake akuchita.+ Pakuti zilizonse zimene Atatewo amachita, Mwana amachitanso zomwezo.
28 Pamenepo Yesu anati: “Mukadzamukweza+ Mwana wa munthu,+ pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine amene munali kumuyembekezera uja,+ ndi kutinso sindichita kanthu mongoganiza ndekha.+ Koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.+
3 Iye amasonyeza ndendende mmene ulemerero wa Mulungu ulili+ ndipo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu weniweniyo,+ ndipo amachirikiza zinthu zonse mwa mawu ake amphamvu.+ Atatiyeretsa potichotsera machimo athu,+ anakhala pansi kudzanja lamanja+ la Wolemekezeka m’malo okwezeka.+