17 Choncho Hananiya anapita ndi kukalowa m’nyumbamo. Ndiyeno anamuika manja n’kunena kuti: “M’bale wanga Saulo, Ambuye Yesu amene waonekera kwa iwe pamsewu umene wadzera, wandituma ine. Wandituma kwa iwe kuti uyambenso kuona ndi kutinso udzazidwe ndi mzimu woyera.”+