14 Iwo anapitiriza ulendo wawo kuchokera ku Pega ndi kukafika ku Antiokeya wa ku Pisidiya. Kumeneko analowa m’sunagoge+ tsiku la sabata ndi kukhala pansi.
14Tsopano Paulo ndi Baranaba ali ku Ikoniyo,+ analowa m’sunagoge+ wa Ayuda. Mmenemo analankhula bwino kwambiri moti khamu lalikulu la Ayuda limodzi ndi Agiriki+ anakhala okhulupirira.