7 Moni kwa Anduroniko ndi Yuniya, omwe ndi achibale anga+ ndi akaidi anzanga.+ Amenewa ndi amuna odziwika kwambiri kwa atumwi ndiponso akhala ogwirizana+ ndi Khristu kwa nthawi yaitali kuposa ine.
30 Koma inu muli ogwirizana ndi Khristu Yesu chifukwa cha Mulunguyo. Yesuyo amatisonyeza nzeru+ za Mulungu ndiponso chilungamo+ cha Mulungu. Kudzera mwa Yesu, anthu akhoza kuyeretsedwa,+ ndipo kudzera mwa dipo* akhoza kumasulidwa,+
14 Pakuti inu abale munatsanzira mipingo ya Mulungu yogwirizana ndi Khristu Yesu imene ili ku Yudeya. Munatero chifukwa inunso munayamba kuvutitsidwa+ ndi anthu akwanu, ngati mmene iwonso akuvutitsidwira ndi Ayuda,