7 Koma osati chabe chifukwa tinali ndi Tito, komanso chifukwa cha mmene inuyo munamulimbikitsira, pamene anatibweretsera uthenga+ wakuti mukufunitsitsa kulapa, muli ndi chisoni, ndiponso mukundidera nkhawa. Nditamva zimenezi ndinakondweranso kwambiri.