38 Pakuti aliyense wochita manyazi ndi ine, komanso ndi mawu anga mu m’badwo wachigololo ndi wochimwa uno, Mwana wa munthu adzachitanso naye manyazi+ akadzafika mu ulemerero wa Atate wake limodzi ndi angelo oyera.”+
14 Ngakhalenso Inoki,+ wa m’badwo wa 7 kuchokera kwa Adamu, analosera za iwowa pamene anati: “Taonani! Yehova anabwera ndi miyandamiyanda ya oyera ake,*+