Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Danieli 7:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “Ndiyeno m’masomphenya ausikuwo, ndinaonanso wina wooneka ngati mwana wa munthu+ akubwera m’mitambo.+ Iye analoledwa kufika kwa Wamasiku Ambiri uja,+ ndipo anamubweretsa pafupi kwambiri ndi Iye.+

  • Mateyu 26:64
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 64 Yesu anamuyankha+ kuti: “Mwanena nokha.+ Ndipo ndikukuuzani anthu inu kuti, kuyambira tsopano+ mudzaona Mwana wa munthu+ atakhala kudzanja lamanja+ lamphamvu. Mudzamuonanso akubwera pamitambo yakumwamba.”+

  • Maliko 13:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Kenako adzaona Mwana wa munthu+ akubwera m’mitambo ndi mphamvu yaikulu ndiponso ulemerero.+

  • Machitidwe 1:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Amunawo anawafunsa kuti: “Amuna inu a ku Galileya, n’chifukwa chiyani muli chilili choncho kuyang’ana kuthambo? Yesu ameneyu, amene watengedwa kupita kumwamba kuchoka pakati panu, adzabwera m’njira yofanana+ ndi mmene mwamuonera akukwera kuthambo.”

  • 1 Atesalonika 4:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pambuyo pake ife amoyo otsalafe, limodzi ndi iwowo,+ tidzatengedwa+ m’mitambo+ kukakumana+ ndi Ambuye m’mlengalenga, ndipo tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.+

  • Chivumbulutso 14:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Nditayang’ana, ndinaona mtambo woyera. Pamtambopo panakhala winawake ngati mwana wa munthu,+ atavala chisoti chachifumu chagolide+ kumutu kwake, chikwakwa chakuthwa chili m’dzanja lake.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena