2 M’masomphenya a Mulungu, iye ananditengera m’dziko la Isiraeli ndi kundikhazika paphiri lalitali kwambiri.+ Mbali ya kum’mwera paphiripo panali chinachake chooneka ngati mzinda.+
2 Ndikudziwa munthu wina wogwirizana ndi Khristu. Zaka 14 zapitazo, munthu ameneyu anakwatulidwira kumwamba kwachitatu. Kaya zimenezo zinachitika ali m’thupi kapena ali kunja kwa thupi sindikudziwa. Akudziwa ndi Mulungu.+