Nyimbo ya Davide ya chikumbutso.
38 Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya,+
Kapena kundilanga mutapsa mtima.+
2 Pakuti mivi yanu yandilasa kwambiri,+
Ndipo dzanja lanu likundilemera.+
3 Palibe pabwino m’thupi langa chifukwa cha chidzudzulo chanu.+
Ndipo m’mafupa anga mulibe mtendere chifukwa cha tchimo langa.+
4 Pakuti zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga.+
Zandilemera kwambiri ngati katundu wolemera.+
5 Zilonda zanga zanunkha ndi kunyeka,
Chifukwa cha kupusa kwanga.+
6 Ndasokonezeka ndipo ndawerama kwambiri chifukwa cha chisoni changa.+
Ndayenda uku ndi uku tsiku lonse ndili wachisoni.+
7 M’chiuno mwanga mukutentha kwambiri,
Ndipo palibe paliponse pabwino m’thupi langa.+
8 Ndalefuka ndipo ndaponderezeka kwambiri.
Ndikulira mofuula chifukwa cha kuvutika kwa mtima wanga.+
9 Inu Yehova, zokhumba zanga zonse zili pamaso panu,
Kudandaula kwanga sikunabisike kwa inu.+
10 Mtima wanga ukugunda kwambiri, ndipo mphamvu zanga zatha,
Maso anga achita mdima.+
11 Anthu amene anali kundikonda ndiponso anzanga aima patali chifukwa cha kuvutika kwanga,+
Ndipo mabwenzi anga apamtima anditalikira.+
12 Anthu amene akufuna kundiwononga anditchera misampha,+
Amene akufuna kundivulaza akulankhula motsutsana nane,+
Ndipo amakhala akukonza zachinyengo tsiku lonse.+
13 Koma ine ndakhala ngati munthu wogontha, sindikumvetsera,+
Ndakhala ngati munthu wosalankhula, sindikutsegula pakamwa.+
14 Ndakhala ngati munthu wosamva,
Sindikulankhula zotsutsana nawo.
15 Pakuti ine ndikuyembekezera inu Yehova.+
Inu Yehova Mulungu wanga, mudzandiyankha.+
16 Ine ndinati: “Ngati simundiyankha adani anga adzasangalala chifukwa cha kusautsika kwanga.+
Phazi langa likaterereka,+ iwo adzadzikweza pamaso panga.”+
17 Ndinali pafupi kupunthwa,+
Ndipo ndinali kumva ululu nthawi zonse.+
18 Pakuti ndinali kulankhula za cholakwa changa.+
Ndipo ndinali kudera nkhawa za tchimo langa.+
19 Adani anga anali amphamvu kwambiri,+
Ndipo odana nane popanda chifukwa anachuluka.+
20 Iwo anali kundibwezera choipa m’malo mwa chabwino,+
Ndikamayesetsa kuchita chabwino anali kunditsutsa.+
21 Inu Yehova, musandisiye.
Inu Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine.+
22 Fulumirani kundithandiza,+
Inu Yehova, chipulumutso changa.+