Masalimo
Salimo la Davide.
א [ʼAʹleph]
ב [Behth]
3 Khulupirira Yehova ndipo chita zabwino.+
Khala padziko lapansi, ndipo khala wokhulupirika m’zochita zako zonse.+
ג [Giʹmel]
6 Iye adzaonetsa poyera kulungama kwako kuti kuunike ngati kuwala,+
Adzaonetsa poyera chilungamo chako kuti chiwale ngati usana.+
ד [Daʹleth]
7 Khala chete pamaso pa Yehova,+
Ndipo umuyembekezere ndi mtima wako wonse.+
Usapse mtima ndi aliyense amene zinthu zikumuyendera bwino,+
Munthu amene akukwaniritsa zolinga zake zoipa.+
ה [Heʼ]
ו [Waw]
10 Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso.+
Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo.+
ז [Zaʹyin]
ח [Chehth]
14 Oipa asolola lupanga ndipo akunga uta wawo,+
Kuti agwetse osautsika ndi osauka,+
Kuti aphe anthu amene njira zawo ndi zowongoka.+
ט [Tehth]
16 Zinthu zochepa za munthu wolungama ndi zabwino+
Kusiyana ndi zinthu zochuluka za anthu ambiri oipa.+
י [Yohdh]
כ [Kaph]
20 Pakuti anthu oipa adzatheratu onse,+
Ndipo adani a Yehova adzafanana ndi busa la msipu wobiriwira mochititsa kaso.
ל [Laʹmedh]
21 Munthu woipa amakongola zinthu za ena koma osabweza,+
Koma wolungama amakomera mtima ena ndipo amapereka mphatso.+
22 Anthu amene Mulungu akuwadalitsa adzalandira dziko lapansi,+
Koma amene wawatemberera adzaphedwa.+
מ [Mem]
נ [Nun]
25 Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula,+
Koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa,+
Kapena ana ake akupemphapempha chakudya.+
26 Tsiku lililonse amakomera mtima ena ndi kuwakongoza zinthu,+
Ndipo ana ake adzalandira madalitso.+
ס [Saʹmekh]
פ [Peʼ]
30 Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula zinthu zanzeru,+
Ndipo lilime lake limalankhula zinthu zachilungamo.+
צ [Tsa·dhehʹ]
33 Koma Yehova sadzasiya wolungama m’manja mwa woipayo,+
Ndipo pamene wolungamayo akuweruzidwa, Mulungu sadzamuona monga wolakwa.+
ק [Qohph]
34 Yembekezera Yehova, ndi kusunga njira zake,+
Ndipo adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi.+
Pamene oipa akuphedwa, iwe udzaona.+
ר [Rehsh]
35 Ine ndaona munthu woipa, wolamulira mwankhanza+
Zinthu zikumuyendera bwino ngati mtengo waukulu wa masamba obiriwira bwino panthaka yake.+
ש [Shin]
37 Ona munthu wosalakwa ndipo yang’anitsitsa munthu wolungama,+
Pakuti tsogolo la munthu ameneyu ndi lamtendere.+
ת [Taw]