Masalimo
ל [Laʹmedh]
10 N’chifukwa chiyani inu Yehova mukuima kutali?+
N’chifukwa chiyani mukubisala pa nthawi ya masautso?+
2 Modzikweza, woipa amathamangitsa wosautsika,+
Ndipo wosautsikayo amakodwa ndi maganizo amene woipa walingalira.+
3 Pakuti woipa amadzitamandira ndi zilakolako zake zadyera,+
Ndipo wopanga phindu lachinyengo+ amadzitamanda.
נ [Nun]
Iye amanyoza Yehova.+
4 Chifukwa cha kutukumuka mtima kwake, woipa safufuza kuti adziwe Mulungu.+
Iye amangoganiza kuti: “Kulibe Mulungu.”+
5 Zochita zake zimayenda bwino nthawi zonse.+
Zigamulo zanu zili pamwamba kwambiri pamene iye sangathe kuziona.+
Onse omuchitira zoipa amawanyodola.+
6 Mumtima mwake amanena kuti: “Sindidzagwedezeka.+
Palibe chimene chidzandichitikira ku mibadwomibadwo.”+
פ [Peʼ]
7 M’kamwa mwake mwadzaza matemberero, chinyengo ndi kupondereza ena.+
Pansi pa lilime lake pamatuluka mavuto ndi zopweteka ena.+
ע [ʽAʹyin]
Maso ake amafunafuna waumphawi.+
9 Amadikirira anthu pamalo obisika ngati mkango pamalo ake obisalapo.+
Amawadikirira+ kuti atenge mokakamiza munthu wosautsika.
Amakulunga wosautsika mu ukonde wake ndi kumutenga mokakamiza.+
10 Wosautsikayo amaponderezedwa, amawerama ndi chisoni,
Ndipo khamu la anthu achisoni limagwera m’manja amphamvu a woipayo.+
11 Mumtima mwake+ amanena kuti: “Mulungu waiwala zochita zanga.+
Wabisa nkhope yake.+
Ndithudi, sadzaona kalikonse.”+
ק [Qohph]
ר [Rehsh]
14 Inu mwaona mavuto ndi masautso.
Mumawayang’anabe kuti muchitepo kanthu.+
Waumphawi,+ mwana wamasiye,* amadziikiza m’manja mwanu.
Inu mwakhala mthandizi wake.+
ש [Shin]
15 Thyolani dzanja la woipa ndi wankhanzayo.+
Fufuzani zoipa zake zonse ndi kumulanga kufikira zoipazo zitatha.+
ת [Taw]