Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo: Iimbidwe chapansipansi.*+ Nyimbo ya Davide.
12 Ndipulumutseni,+ inu Yehova, pakuti anthu okhulupirika atha.+
Anthu okhulupirika atheratu pakati pa ana a anthu.
3 Yehova adzadula milomo yonse yolankhula zachinyengo
Ndi lilime lolankhula modzikuza.+
4 Iye adzadula anthu onena kuti: “Ndi lilime lathu tidzapambana.+
Timalankhula chilichonse chimene tikufuna ndi milomo yathu. Ndani angatilamulire?”
5 Tsopano Yehova wanena kuti: “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa osautsika, chifukwa cha kuusa moyo kwa anthu osauka,+
Ndidzanyamuka pa nthawiyo,+
Ndidzawateteza kwa aliyense wowanyodola.”+