Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe chapansipansi* ndi zoimbira za zingwe.+ Nyimbo ya Davide.
2 Ndikomereni mtima, inu Yehova, chifukwa ndikulefuka.+
Ndichiritseni,+ inu Yehova, chifukwa mafupa anga agwedezeka.
4 Bwererani+ mudzapulumutse moyo wanga, inu Yehova.+
Ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha.+
6 Ndalefuka chifukwa cha kuusa moyo* kwanga.+
Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa.+
Ndimakhathamitsa bedi langa ndi misozi.+
7 Maso anga achita mdima chifukwa cha chisoni changa.+
Maso anga akalamba chifukwa cha anthu onse ondichitira zoipa.+