Masalimo
2 Mundilanditse chifukwa cha chilungamo chanu ndipo mundipulumutse.+
Tcherani khutu lanu kwa ine ndi kundipulumutsa.+
3 Mukhale thanthwe lachitetezo loti ndizilowamo nthawi zonse.+
Lamulani kuti ndipulumutsidwe,+
Pakuti inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+
4 Inu Mulungu wanga, ndipulumutseni m’manja mwa woipa,+
Ndipulumutseni m’manja mwa munthu wochita zinthu mopanda chilungamo komanso mopondereza.+
5 Pakuti chiyembekezo changa ndinu,+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, ndimadalira inu kuyambira pa unyamata wanga.+
6 Kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga inu mwandithandiza.+
Inu ndi amene munanditulutsa m’mimba mwa mayi anga.+
Ndimatamanda inu nthawi zonse.+
8 M’kamwa mwanga mwadzaza mawu otamanda inu,+
Ndipo pakamwa panga pakunena za ulemerero wanu tsiku lonse.+
10 Pakuti adani anga anena za ine,+
Ndipo anthu olondalonda moyo wanga, onse pamodzi achita upo,+
11 Iwo akunena kuti: “Mulungu wamusiya.+
Mulondoleni ndi kumugwira pakuti palibe womulanditsa.”+
13 Anthu otsutsana nane achite manyazi, iwo awonongedwe.+
Amene akufunafuna kundigwetsera tsoka adziphimbe ndi chitonzo ndiponso manyazi.+
15 Pakamwa panga padzanena za chilungamo chanu,+
Padzanena za chipulumutso chanu tsiku lonse,+
Pakuti ntchito za chilungamo ndi chipulumutso chanu ndi zochuluka ndipo sindinathe kuziwerenga.+
16 Ndidzabwera ndi kunena za mphamvu zanu zazikulu,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+
Ndidzanena za chilungamo chanu, osati cha wina aliyense.+
17 Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira pa unyamata wanga,+
Ndipo mpaka pano ndikunena za ntchito zanu zodabwitsa.+
18 Ngakhale nditakalamba ndi kumera imvi, inu Mulungu musandisiye,+
Kufikira nditanena za dzanja lanu lamphamvu ku m’badwo wotsatira,+
Kufikira nditanena za mphamvu zanu kwa onse obwera m’tsogolo.+
19 Chilungamo chanu, inu Mulungu chafika kumwamba.+
Tikanena za zinthu zazikulu zimene munachita,+
Inu Mulungu, ndani angafanane ndi inu?+
20 Chifukwa chakuti mwandionetsa masautso ndi masoka ambiri,+
Nditsitsimutseni.+
Nditulutseninso m’madzi akuya, pansi pa nthaka.+
22 Inenso ndidzakutamandani ndi chipangizo cha zingwe,+
Ndidzatamanda choonadi chanu, inu Mulungu.+
Ndidzaimba nyimbo zokutamandani ndi zeze, Inu Woyera wa Isiraeli.+