Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
21 Inu Yehova, mfumu ikukondwera mu mphamvu zanu.+
Ndipo idzapitiriza kukondwera mu chipulumutso chanu.+
3 Munaidalitsa ndi kuipatsa zinthu zabwino,+
Ndipo pamutu pake munaika chisoti chachifumu chagolide woyengeka bwino.+
4 Mfumuyo inakupemphani moyo. Ndipo munaipatsadi,+
Munaipatsa masiku ochuluka kuti ikhale mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+
6 Mwaichititsa kukhala yodalitsika kwambiri mpaka muyaya.+
Mwaikondweretsa ndi kuisangalatsa pamaso panu.+
7 Pakuti mfumu imakhulupirira Yehova,+
Imakhulupirira kukoma mtima kosatha kwa Wam’mwambamwamba. Iyo siidzagwedezeka.+
9 Mudzawakhalitsa ngati oponyedwa mung’anjo yamoto pa nthawi ya kuonekera kwanu.+
Yehova adzawameza mu mkwiyo wake, ndipo moto udzawanyeketsa.+
10 Mudzawononga ana awo kuwachotsa padziko lapansi,+
Ndipo ana awo mudzawachotsa pakati pa ana a anthu.+