Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
132 Inu Yehova, kumbukirani Davide,+
Kumbukirani masautso ake onse.+
2 Kumbukirani kuti analumbira kwa inu Yehova,+
Analonjeza kwa Wamphamvu+ wa Yakobo kuti:+
3 “Sindilowa m’nyumba yanga.+
Sindigona pabedi langa.+
4 Maso anga saona tulo,+
Ndipo sindilola maso anga owala kuwodzera,+
5 Kufikira Yehova nditamupezera nyumba,+
Kufikira nditapeza chihema chachikulu cha Wamphamvu wa Yakobo.”+
6 Taonani! Tamva za Likasa ku Efurata,+
Talipeza kunkhalango.+
7 Tiyeni tilowe m’chihema chake chachikulu.+
Tiyeni tiwerame pachopondapo mapazi ake.+
8 Nyamukani, inu Yehova, kuti mulowe kumalo anu okhalamo,+
Inu pamodzi ndi Likasa+ limene mumasonyezera mphamvu zanu.+
9 Ansembe anu avale chilungamo,+
Ndipo okhulupirika anu afuule mosangalala.+
10 Chifukwa cha zimene munalonjeza Davide mtumiki wanu,+
Musakane kuona nkhope ya wodzozedwa wanu.+
11 Yehova walumbira kwa Davide,+
Ndithudi sadzabweza mawu ake akuti:+
“Ndidzaika pampando wako wachifumu+
Chipatso cha mimba yako.+
12 Ana ako akadzasunga pangano langa+
Ndi zikumbutso zanga zimene ndidzawapatsa,+
Ngakhalenso ana awo+
Adzakhala pampando wako wachifumu kwamuyaya.”+
13 Yehova wasankha Ziyoni,+
Ndipo amafunitsitsa kuti akhale malo ake okhalamo. Iye amati:+
14 “Awa ndi malo anga okhalamo mpaka muyaya.+
Ndidzakhala mmenemu, pakuti ndimafunitsitsa kukhala m’malo amenewa.+
15 Ndithu ndidzadalitsa chakudya chake.+
Anthu ake osauka ndidzawapatsa chakudya chokwanira.+
16 Ansembe ake ndidzawaveka chipulumutso,+
Ndipo anthu ake okhulupirika adzafuula ndithu mokondwera.
17 Ku Ziyoniko ndidzakulitsa nyanga ya Davide.+
Wodzozedwa wanga ndamukonzera nyale.+
18 Adani ake ndidzawaveka manyazi,+
Koma ufumu+ wake udzapita patsogolo.”+