Salimo
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
132 Inu Yehova, kumbukirani Davide
Komanso mavuto onse amene anakumana nawo.+
2 Kumbukirani kuti analumbira kwa inu Yehova,
Analonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti:+
3 “Sindidzalowa mutenti yanga, mʼnyumba yanga.+
Sindidzagona pabedi langa.
4 Sindidzalola kuti ndigone
Kapena kutseka maso anga,
5 Mpaka nditamupezera Yehova malo okhala,
8 Nyamukani, inu Yehova, kuti mulowe mʼmalo anu okhalamo,+
Inu pamodzi ndi Likasa limene likuimira mphamvu zanu.+
9 Ansembe anu avale chilungamo,
Ndipo okhulupirika anu afuule mosangalala.
11 Yehova walumbira kwa Davide.
Ndithudi sadzalephera kukwaniritsa mawu ake akuti:
12 Ana ako akadzasunga pangano langa
Komanso malamulo* anga amene ndikuwaphunzitsa,+
Ana awonso
Adzakhala pampando wako wachifumu kwamuyaya.”+
14 “Awa ndi malo anga okhalamo mpaka kalekale.
Ndidzakhala mmenemu,+ chifukwa zimenezi ndi zimene ndikulakalaka.
15 Ndidzadalitsa kwambiri malo amenewa ndi chakudya.
Anthu ake osauka ndidzawapatsa chakudya chokwanira.+
17 Kumeneko ndidzachulukitsa mphamvu* za Davide.
Wodzozedwa wanga ndamukonzera nyale.+