Masalimo
Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora. Kwa wotsogolera nyimbo pa Mahalati.* Iimbidwe molandizana. Masikili* ya Hemani+ wa m’banja la Zera.
88 Inu Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa,+
Masana ndimafuula kwa inu,+
Usikunso ndimafuula pamaso panu.+
4 Anandiika m’gulu la anthu otsikira kudzenje.+
Ndakhala ngati mwamuna wanyonga zake koma wopanda mphamvu.+
5 Ndakhala womasuka ngati anthu akufa,+
Ngati anthu ophedwa amene agona m’manda,+
Anthu amene simukuwakumbukiranso
Komanso amene sakulandira thandizo kuchokera m’manja mwanu.+
8 Anzanga mwawaika kutali ndi ine.+
Mwandisandutsa chinthu chonyansa kwa iwo.+
Ndatsekerezedwa ndipo sindingathenso kuchoka.+
9 Diso langa lafooka chifukwa cha kusautsika kwanga.+
Ndaitana inu Yehova tsiku lonse.+
Ndapemphera kwa inu nditakweza manja anga.+
10 Kodi anthu akufa mudzawachitira zodabwitsa?+
Kapena kodi anthu akufa, anthu amene sangachite kanthu, adzauka?+
Kodi adzakutamandani?+ [Seʹlah.]
11 Kodi adzalengeza za kukoma mtima kwanu kosatha m’manda?
Kodi adzalengeza za kukhulupirika kwanu m’malo a chiwonongeko?+
12 Kodi zodabwitsa zimene inu mukuchita zidzadziwika mu mdima?+
Kapena kodi chilungamo chanu chidzadziwika m’dziko la anthu oiwalika?+
13 Koma ine ndafuulira inu Yehova kupempha thandizo,+
Ndipo m’mawa mapemphero anga amafika kwa inu nthawi zonse.+
15 Kuyambira pa unyamata wanga ndakhala ndikusautsika komanso kutsala pang’ono kufa.+
Ndapirira kwambiri zinthu zoopsa zochokera kwa inu.+