Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo pa Yedutuni. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
2 Pa tsiku la zowawa zanga ndafunafuna Yehova.+
Ndakweza dzanja langa kumwamba usiku wonse, ndipo silinachite dzanzi.
Koma sindinatonthozeke.+
3 Ndidzakumbukira Mulungu ndipo ndidzavutika maganizo.+
Ine ndasautsika. N’chifukwa chake ndafooka.+ [Seʹlah.]
6 Usiku ndidzakumbukira nyimbo zanga zoimbidwa ndi chipangizo cha zingwe.+
Ndidzasonyeza kudera nkhawa mumtima mwanga,+
Ndipo ndidzasinkhasinkha zinthu zonse mozama.
8 Kodi kukoma mtima kwake kosatha wakusiya mpaka muyaya?+
Kodi malonjezo ake sadzakwaniritsidwa+ ku mibadwomibadwo?
10 Kodi ndizingonena kuti: “Zimene zikundisautsa n’zakuti,+
Wam’mwambamwamba wasiya kutipatsa thandizo”?+
13 Inu Mulungu, njira yanu ili m’malo oyera.+
Kodi ndi Mulungu wamkulu uti amene angafanane ndi Mulungu wathu?+
14 Inu ndinu Mulungu woona amene mukuchita zodabwitsa.+
Mphamvu zanu mwazidziwikitsa pakati pa mitundu ya anthu.+
16 Madzi akuonani, inu Mulungu,
Madzi akuonani, ndipo ayamba kumva ululu woopsa.+
Komanso madzi akuya ayamba kuwinduka.+
17 Mitambo yatulutsa mabingu ndi kugwetsa madzi.+
Thambo latulutsa mkokomo.
Mphezi zanu zinawala paliponse ngati mivi.+
18 Phokoso la bingu lanu linali ngati la mawilo a galeta.+
Mphezi zinaunika padziko.+
Ndipo dziko lapansi linagwedezeka ndi kuyamba kunjenjemera.+