Masalimo
Tamandani dzina la Yehova,+
Mutamandeni, inu atumiki a Yehova,+
2 Inu amene mukuimirira m’nyumba ya Yehova,+
M’mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.+
3 Tamandani Ya, pakuti Yehova ndi wabwino.+
Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti kuchita zimenezi n’kosangalatsa.+
6 Chilichonse chimene Yehova anafuna kuchita anachita.+
Anachita zimenezi kumwamba, padziko lapansi, m’nyanja ndi m’madzi onse akuya.+
7 Amachititsa nthunzi kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
Iye anapanganso zipata zotulukirapo mvula.+
Amachititsa mphepo kutuluka m’nkhokwe zake.+
8 Wochita zimenezi ndiye anapha ana oyamba kubadwa a ku Iguputo,+
Anapha ana a anthu ngakhalenso ana a nyama.+
9 Anasonyeza zizindikiro ndi kuchita zozizwitsa pakati pako Iguputo iwe,+
Anachita zimenezo kwa Farao ndi kwa atumiki ake onse.+
10 Amene anachita zimenezi ndi amene anakantha mitundu yambiri+
Ndi kupha mafumu amphamvu.+
11 Anaphanso Sihoni mfumu ya Aamori+
Ndi Ogi mfumu ya Basana,+
Ndipo anafafaniza maufumu onse a ku Kanani.+
12 Dziko lawo analipereka kukhala cholowa,+
Cholowa cha anthu ake Aisiraeli.+
15 Mafano a anthu a mitundu ina ndi opangidwa ndi siliva ndi golide,+
Ntchito ya manja a munthu wochokera kufumbi.+