Masalimo
2 Imbirani Yehova, tamandani dzina lake.+
Tsiku ndi tsiku lengezani uthenga wabwino wa chipulumutso chake.+
3 Lengezani ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina,+
Ndiponso ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.+
4 Pakuti Yehova ndi wamkulu+ ndi woyenera kutamandidwa kwambiri.
Iye ndi wochititsa mantha kuposa milungu ina yonse.+
5 Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake,+
Koma Yehova ndiye anapanga kumwamba.+
7 Vomerezani Yehova, inu mabanja a mitundu ya anthu,+
M’patseni Yehova ulemerero ndi kuvomereza kuti iye ndi wamphamvu.+
9 Gwadirani Yehova mutavala zovala zokongola ndi zopatulika.+
Njenjemerani ndi mantha aakulu* pamaso pake, inu anthu nonse okhala padziko lapansi.+
10 Nenani pakati pa anthu a mitundu ina kuti: “Yehova wakhala mfumu.+
Dziko lapansi nalonso lakhazikika moti silingagwedezeke.+
Iye adzaweruzira mitundu ya anthu milandu yawo mwachilungamo.”+