Nahumu
1 Uwu ndi uthenga wokhudza Nineve:+ Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi:
2 Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha+ ndipo amabwezera adani ake.+ Yehova amabwezera adani ake ndipo ndi waukali.+ Yehova amabwezera adani ake+ ndipo saiwala zoipa zimene iwo anachita.+
3 Yehova sakwiya msanga+ ndipo ali ndi mphamvu zambiri,+ komatu Yehova salephera kulanga wolakwa.+
Njira yake ili mumphepo yowononga ndi mumphepo yamkuntho. Mitambo ndilo fumbi lopondapo mapazi ake.+
4 Amadzudzula nyanja+ ndi kuiphwetsa ndipo amaumitsa mitsinje yonse.+
Basana ndi Karimeli afota+ ndipo maluwa a mitengo ya ku Lebanoni nawonso afota.
5 Mapiri agwedezeka chifukwa cha iye ndipo zitunda zasungunuka.+
Dziko lapansi, nthaka ndi zinthu zonse zokhala m’dzikomo zidzanjenjemera.+
6 Iye atapsa mtima, ndani angaime pamaso pake?+ Iye atakwiya, ndani angalimbe mtima kuima pamaso pake?+
Mkwiyo wake adzaukhuthula ngati moto+ ndipo miyala idzagwetsedwa chifukwa cha iye.
7 Yehova ndi wabwino+ ndipo ndi malo achitetezo+ pa tsiku la nsautso.+
Amadziwa amene amathawira kwa iye kuti apeze chitetezo.+
8 Adzafafaniza mzinda umenewo+ ndi madzi osefukira ndipo mdima udzathamangitsa adani ake.+
9 Kodi anthu inu mungakonze chiwembu chotani kuti muukire Yehova?+ Iye adzakufafanizani moti simudzakhalaponso.
Sipadzakhalanso nsautso.+
10 Ngakhale kuti iwo alukanalukana ngati minga+ ndipo aledzera ngati kuti amwa mowa,+ adzatenthedwa ngati mapesi ouma.+
11 Mwa iwe mudzatuluka wina amene akuganiza zochitira Yehova zoipa+ ndi kulangiza anthu zinthu zopanda pake.+
12 Yehova wanena kuti: “Ngakhale kuti iwo anali achikwanekwane ndiponso anali ndi mphamvu zambiri, adzadulidwa+ ndipo wina adzawaukira. Pamenepo ndidzakusautsa kufikira pamene sudzafunikiranso kusautsidwa.+ 13 Tsopano ndidzathyola goli lake lonyamulira katundu ndi kulichotsa pa iwe,+ ndipo ndidzadula zingwe zimene anakumanga nazo.+ 14 Koma ponena za iwe, Yehova walamula kuti, ‘Sudzakhalanso ndi ana otchedwa ndi dzina lako.+ Ndidzadula zifaniziro zosema ndi zifaniziro zopangidwa ndi chitsulo chosungunula+ ndipo ndidzazitaya kunja kwa nyumba za milungu yako. Ndidzakukonzera manda+ chifukwa ndiwe wopanda pake.’
15 “Taonani mapazi a munthu yemwe akuyenda pamwamba pa mapiri pobweretsa uthenga wabwino.+ Iye akulengeza za mtendere. Iwe Yuda, chita zikondwerero zako.+ Kwaniritsa zimene walonjeza+ chifukwa palibe munthu aliyense wopanda pake amene adzadutsa pakati pako.+ Munthu wopanda pakeyo adzaphedwa.”+