Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora.+ Masikili.*
44 Inu Mulungu, ife tamva ndi makutu athu,
Makolo athu anatifotokozera+
Ntchito zimene inu munachita m’masiku awo,+
M’masiku akale.+
2 Munapitikitsa anthu a mitundu ina ndi dzanja lanu,+
Ndipo m’malo mwawo munakhazikitsa anthu anu.+
Munagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuipitikitsa.+
3 Pakuti iwo sanatenge dzikolo chifukwa cha lupanga lawo,+
Ndipo si mkono wawo umene unawabweretsera chipulumutso.+
Koma chinabwera ndi dzanja lanu lamanja,+ mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,
Chifukwa munakondwera nawo.+
7 Ndinu amene munatipulumutsa kwa adani athu,+
Ndipo munanyazitsa anthu amene amadana nafe kwambiri.+
10 Mwachititsa kuti tithawe pamaso pa adani athu,+
Ndipo anthu odana nafe kwambiri afunkha zinthu zathu.+
11 Mwatipereka kwa adani athu kuti atidye ngati nkhosa,+
Ndipo mwatimwaza pakati pa anthu a mitundu ina.+
13 Mwatisandutsa chitonzo kwa anthu oyandikana nafe,+
Mwatisandutsa chinthu chonyozeka ndi choseketsa kwa onse otizungulira.+
14 Mwatisandutsa mwambi pakati pa anthu a mitundu ina,+
Mwatisandutsa anthu amene anthu a mitundu inawo akuwapukusira mitu.+
15 Zondichititsa manyazi zili pamaso panga tsiku lonse,
Ndipo manyazi aphimba nkhope yanga,+
16 Chifukwa cha mawu a munthu wonditonza ndi wolankhula zachipongwe,
Ndiponso chifukwa cha mdani wanga ndi wofuna kundibwezera choipa.+
18 Mitima yathu sinakhale yosakhulupirika n’kuchoka panjira yanu,+
Ndipo mapazi athu sanapatuke panjira yanu.+
20 Ngati tikanaiwala dzina la Mulungu wathu,
Kapena kupemphera kwa mulungu wachilendo titakweza manja athu,+
21 Kodi Mulungu sakanafufuza zimenezi?+
Pakuti iye amadziwa zinsinsi za mumtima.+