Masalimo
Nyimbo ya Davide.
15 Inu Yehova, ndani amene angakhale mlendo m’chihema chanu?+
Ndani angakhale m’phiri lanu lopatulika?+
2 Ndi amene akuyenda mosalakwitsa zinthu,+ amene amachita chilungamo,+
Ndi kulankhula zoona mumtima mwake.+
3 Iye sanena miseche ndi lilime lake.+
Sachitira mnzake choipa,+
Ndipo satonza bwenzi lake lapamtima.+