Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda.
122 Ndinakondwera pamene anandiuza kuti:+
“Tiyeni tipite+ kunyumba ya Yehova.”+
2 Mapazi athu anaima+
Pazipata zako iwe Yerusalemu.+
3 Mzinda wa Yerusalemu unamangidwa+
Ngati chinthu chimodzi chogwirizana,+
4 Mafuko amapita kumeneko,+
Mafuko a Ya,+
Amapita kumeneko kukatamanda dzina la Yehova+
Mogwirizana ndi lamulo loperekedwa kwa Isiraeli.+
5 Kumeneko n’kumene kumakhala mipando yachiweruzo,+
Mipando yachifumu ya nyumba ya Davide.+
6 Pemphererani mtendere wa Yerusalemu, anthu inu.+
Amene amakukonda, mzinda iwe, sadzakhala ndi nkhawa iliyonse.+
7 M’malo ako otchingidwa ndi khoma lolimba mupitirizebe kukhala mtendere,+
Anthu okhala munsanja zako apitirizebe kukhala opanda nkhawa iliyonse.+
8 Tsopano ndikulankhula m’malo mwa abale anga ndi anzanga kuti:+
“Mtendere ukhale nawe.”+
9 Chifukwa cha nyumba ya Yehova Mulungu wathu,+
Ndidzapitiriza kukupempherera kuti zinthu zikuyendere bwino.+