Zekariya
4 Mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja anabwerera n’kundidzutsa, ndipo ndinadzuka ngati munthu amene anali kugona.+ 2 Kenako anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani?”+
Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona choikapo nyale chagolide yekhayekha.+ Pamwamba pake pali mbale yolowa. Choikapo nyalecho chili ndi nyale 7, inde, nyale 7.+ Nyale zimene zili pachoikapo nyalecho, zili ndi mapaipi 7. 3 M’mbali mwa choikapo nyalecho muli mitengo iwiri ya maolivi.+ Umodzi uli mbali ya kudzanja lamanja la mbale yolowayo, ndipo wina uli kumanzere kwa mbaleyo.”
4 Kenako ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja kuti: “Kodi zimenezi zikuimira chiyani mbuyanga?”+ 5 Mngeloyo anandiyankha kuti: “Kodi sukudziwadi tanthauzo la zinthu zimenezi?”
Pamenepo ine ndinati: “Inde sindikudziwa mbuyanga.”+
6 Choncho iye anandiuza kuti: “Yehova wauza Zerubabele kuti, ‘“Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo,+ kapena mphamvu,+ koma mzimu wanga,”+ watero Yehova wa makamu. 7 Ngakhale pataikidwa chopinga chachikulu ngati phiri+ pamaso pa Zerubabele,+ chidzasalazidwa kukhala malo athyathyathya. Ndithu iye adzabweretsa mwala wotsiriza wa pakona.+ Akadzatero anthu adzafuula+ kuti: “Koma mwalawu ndiye ndi wokongola bwanji! Koma ndiye ndi wokongola!”’”+
8 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 9 “Manja a Zerubabele anayala maziko a nyumbayi,+ ndipo manja ake omwewo adzaimalizitsa.+ Pamenepo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma kwa inu.+ 10 Munthu asakunyozeni chifukwa chakuti munayamba kumanga ndi zinthu zochepa.+ Anthu adzasangalala ndi ntchito imeneyi+ ndipo adzaona chingwe cha mmisiri womanga nyumba m’dzanja la Zerubabele. Maso 7 adzaona zimenezi. Maso 7 amenewa ndiwo maso a Yehova,+ ndipo akuyang’ana uku ndi uku padziko lonse lapansi.”+
11 Ndiyeno ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja kuti: “Kodi mitengo iwiri ya maolivi, imene wina uli kudzanja lamanja ndi wina kumanzere kwa choikapo nyalechi, ikuimira chiyani?”+ 12 Ndinamufunsanso kuti: “Kodi nthambi ziwiri izi za mitengo ya maolivi, zimene zikuthira mafuta agolide m’mbale yolowa kudzera m’mapaipi awiri agolide, zikuimira chiyani?”
13 Iye anandiyankha kuti: “Kodi sukudziwadi tanthauzo la zinthu zimenezi?”
Pamenepo ine ndinati: “Inde sindikudziwa mbuyanga.”+
14 Ndipo iye anandiuza kuti: “Zinthu zimenezi zikuimira odzozedwa awiri+ amene amaimirira kumbali iyi ndi mbali inayi ya Ambuye wa dziko lonse lapansi.”+