148 Tamandani Ya, anthu inu!+
Tamandani Yehova inu okhala kumwamba.+
Mutamandeni inu okhala m’mwamba.+
2 Mutamandeni, inu angelo ake onse.+
Mutamandeni, inu khamu lake lonse.+
3 Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi.+
Mutamandeni, inu nyenyezi zonse zowala.+
4 Mutamandeni, inu kumwamba kwa m’mwambamwamba,+
Ndi inunso madzi okhala pamwamba pa miyamba.+
5 Zonsezi zitamande dzina la Yehova,+
Pakuti iye analamula ndipo zinalengedwa.+
6 Amazichititsa kukhalapobe kwamuyaya, ngakhalenso mpaka kalekale.+
Iye wazikhazikitsira lamulo, ndipo silidzatha.+
7 Tamandani Yehova, inu okhala padziko lapansi,+
Inu zilombo za m’nyanja ndi inu nonse madzi akuya,+
8 Inu moto ndi matalala, chipale chofewa ndi utsi wakuda bii,+
Iwe mphepo yamkuntho yokwaniritsa mawu ake.+
9 Mutamandeni inu mapiri ndi inu nonse zitunda,+
Inu mitengo ya zipatso ndi inu nonse mitengo ya mkungudza.+
10 Inu nyama zakutchire ndi inu nonse nyama zoweta,+
Inu zinthu zokwawa ndi mbalame zamapiko.+
11 Mutamandeni inu mafumu a padziko lapansi+ ndi inu nonse mitundu ya anthu,
Inunso akalonga+ ndi inu nonse oweruza a padziko lapansi,+
12 Inu anyamata+ ndi inunso anamwali,+
Inu okalamba+ pamodzi ndi ana.+
13 Onse, anthu ndi nyama, atamande dzina la Yehova,+
Pakuti dzina lake lokhalo lili pamwamba posafikirika.+
Ulemerero wake uli pamwamba kuposa dziko lapansi ndi kumwamba.+
14 Iye adzakweza nyanga ya anthu ake.+
Adzachititsa kuti anthu ake onse okhulupirika atamandike,+
Amene ndi ana a Isiraeli, anthu amene ali pafupi ndi iye.+
Tamandani Ya, anthu inu!+