Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+
48 Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri,+
Mumzinda wa Mulungu wathu,+ m’phiri lake loyera.+
2 Phiri la Ziyoni limene lili m’dera lakutali la kumpoto,+
Ndi lokongola chifukwa lili pamalo okwezeka ndi osangalatsa padziko lonse lapansi,+
Mudzi wa Mfumu Yaikulu.+
3 Munsanja zokhalamo za m’mudzimo, Mulungu wadziwika kuti ndi malo okwezeka ndiponso achitetezo.+
4 Taonani! Mafumu anakumana atapangana,+
Koma anangodutsa.+
5 Iwo anaona ndipo anadabwa.
Anasokonezeka, moti anathawa mopanikizika kwambiri.+
6 Kumeneko iwo anayamba kunjenjemera,+
Anamva zopweteka ngati za mkazi amene akubereka.+
7 Pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu ya kum’mawa, munaswa zombo za ku Tarisi.+
8 Ife taona zimene Mulungu anachita monga mmene tinamvera,+
Mumzinda wa Yehova wa makamu, mumzinda wa Mulungu wathu.+
Mulungu adzakhazikitsa mzindawo mpaka kalekale.+ [Seʹlah.]
9 Inu Mulungu, ife talingalira mozama za kukoma mtima kwanu kosatha,+
Tili mkati mwa kachisi wanu.+
10 Inu Mulungu, mofanana ndi dzina lanu,+ kukutamandani
Kwafika kumalire a dziko lapansi.
Dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.+
11 Phiri la Ziyoni+ likondwere,
Midzi yozungulira Yuda isangalale+ chifukwa cha zigamulo zanu.+
12 Gubani mozungulira Ziyoni, anthu inu, ndipo yendayendani mmenemo,+
Werengani nsanja zake.+
13 Ganizirani mofatsa za khoma lake lolimba.+
Yenderani nsanja zake zokhalamo,
Kuti mudzasimbire m’badwo wam’tsogolo.+
14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+
Iye adzatitsogolera kufikira imfa yathu.+