Yobu
25 Tsopano Bilidadi+ wa ku Shuwa anayankha kuti:
2 “Ulamuliro ndi wake ndipo iye ndi wochititsa mantha.+
Iye amakhazikitsa mtendere kumwamba.
3 Kodi asilikali ake angatheke kuwawerenga?
Ndipo ndani amene kuwala kwake sikum’fika?
4 Choncho, kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu?+
Kapena kodi munthu wobadwa kwa mkazi angakhale bwanji woyera?+
5 Kulitu mwezi koma si wowala.
Ndipo nyenyezi si zoyera m’maso mwake.