Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+
49 Mvetserani izi, anthu nonsenu.
Tcherani khutu inu nonse a m’nthawi* ino,+
2 Inu mtundu wa anthu ndiponso inu ana a anthu,
Inu olemera pamodzi ndi inu osauka.+
3 Pakamwa panga padzalankhula zinthu zanzeru,+
Ndipo zosinkhasinkha za mtima wanga zidzakhala zinthu zakuya.+
6 Anthu amene akukhulupirira chuma chawo,+
Amene akudzitamandira chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chawo,+
7 Palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene angathe kuwombola m’bale wake,+
Kapena kumuperekera dipo* kwa Mulungu,
8 (Ndipo malipiro owombolera moyo wawo ndi amtengo wapatali,+
Moti munthu sangathe kuwapereka mpaka kalekale)
9 Kuti akhale ndi moyo mpaka muyaya osaona dzenje la manda.+
10 Pakuti amaona kuti ngakhale anthu anzeru amafa,+
Wopusa ndi wopanda nzeru, onsewo amawonongeka,+
Ndipo chuma chawo amasiyira anthu ena.+
11 Zokhumba za mtima wawo n’zakuti nyumba zawo zikhalebe mpaka kalekale,+
Mahema awo akhalebe ku mibadwomibadwo.+
Malo awo amawatcha mayina awo.+
12 Komabe munthu wochokera kufumbi, ngakhale atakhala wolemekezeka, sangakhale ndi moyo mpaka kalekale.+
Iye amangofanana ndi nyama zimene zaphedwa.+
13 Umu ndi mmene zimakhalira ndi zitsiru,+
Komanso amene amazitsanzira, omwe amasangalala ndi mawu awo odzitukumula. [Seʹlah.]
14 Awatsogolera ku Manda ngati nkhosa zopita kokaphedwa.+
Imfa idzakhala m’busa wawo.+
Ndipo m’mawa anthu owongoka mtima adzawalamulira.+
Matupi awo adzawonongeka.+
Aliyense wa iwo malo ake okhala ndi ku Manda, osati malo okwezeka.+
16 Musachite mantha chifukwa chakuti munthu wina akupeza chuma,+
Kapena chifukwa chakuti ulemerero wa nyumba yake ukuwonjezeka,+
17 Pakuti pa imfa yake sangatenge kena kalikonse.+
Ulemerero wake sudzapita naye pamodzi.+