Masalimo
Nyimbo ya Asafu.
79 Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowa m’dziko limene ndilo cholowa chanu.+
Aipitsa kachisi wanu woyera.+
Awononga Yerusalemu ndi kumusandutsa bwinja.+
2 Apereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame kuti chikhale chakudya chawo.+
Matupi a okhulupirika anu awapereka kwa zilombo zakutchire.+
5 Haa! Inu Yehova, mukhala wokwiya mpaka liti? Kwamuyaya?+
Kodi mkwiyo wanu udzakhala ukuyaka ngati moto mpaka liti?+
6 Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu amene akukunyalanyazani,+
Ndi pa maufumu amene sakuitana pa dzina lanu.+
8 Musatiimbe mlandu chifukwa cha zolakwa za makolo athu.+
Fulumirani! Tisonyezeni chifundo chanu,+
Chifukwa tasautsika koopsa.+
9 Tithandizeni inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+
Kuti dzina lanu lilemekezedwe.+
Tipulumutseni ndi kutikhululukira* machimo athu chifukwa cha dzina lanu.+
10 Musalole kuti anthu a mitundu ina azinena kuti: “Mulungu wawo ali kuti?”+
Pamene mukubwezera anthu a mitundu inawo chifukwa cha magazi a atumiki anu amene anakhetsedwa,+
Ife tidzaone ndi maso athu.+