Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.
85 Inu Yehova, mwasangalala ndi dziko lanu.+
Mwabwezeretsa ana a Yakobo amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.+
2 Mwakhululukira anthu anu zolakwa zawo.+
Mwaphimba machimo awo onse.+ [Seʹlah.]
3 Mwalamulira mkwiyo wanu wonse,+
Ndipo simunasonyeze kutentha kwa mkwiyo wanu.+
4 Tisonkhanitseni ndi kutibwezeretsa mwakale, inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+
Ndipo tichotsereni mkwiyo wanu.+
5 Kodi mupitiriza kutikwiyira mpaka kalekale?+
Kodi mudzasonyeza mkwiyo wanu ku mibadwomibadwo?+
6 Kodi simutitsitsimutsanso+
Kuti anthu anu akondwere chifukwa cha inu?+
7 Inu Yehova, tisonyezeni kukoma mtima kwanu kosatha,+
Ndipo tipatseni chipulumutso chanu.+
8 Ndidzamvetsera zimene Mulungu woona Yehova adzanena,+
Pakuti adzanena za mtendere kwa anthu ake+ ndi kwa okhulupirika ake.
Koma iwo asadzidalire kwambiri ngati kale.+
9 Ndithudi, chipulumutso chake chili pafupi ndi amene amamuopa,+
Kuti ulemerero ukhale m’dziko lathu.+
10 Kukoma mtima kosatha ndi choonadi zakumana.+
Chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.+
11 Choonadi chidzaphuka padziko lapansi,+
Ndipo chilungamo chidzayang’ana pansi kuchokera kumwamba.+
12 Yehova nayenso adzapereka zinthu zabwino,+
Ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.+
13 Chilungamo chidzayenda pamaso pake,+
Ndipo chidzapanga njira yotsatira mapazi a Mulungu.+