Masalimo
Pemphero la Davide.
2 Tetezani moyo wanga pakuti ndine wokhulupirika.+
Inu ndinu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu amene amakukhulupirirani.+
5 Pakuti inu Yehova ndinu Mulungu wabwino+ ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.+
Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.+
8 Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu.+
Ndipo palibe ntchito zilizonse zofanana ndi ntchito zanu.+
9 Mitundu yonse imene munapanga idzabwera kwa inu,+
Ndipo idzagwada pamaso panu, inu Yehova,+
Ndi kulemekeza dzina lanu.+
11 Inu Yehova, ndilangizeni za njira yanu.+
Ndidzayenda m’choonadi chanu.+
Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.+
12 Ndikukutamandani inu Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse,+
Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale,
13 Pakuti kukoma mtima kosatha kumene mwandisonyeza ndi kwakukulu,+
Ndipo mwapulumutsa moyo wanga ku Manda, kumalo apansi penipeni.+
14 Inu Mulungu, anthu odzitukumula andiukira.+
Khamu la anthu opondereza anzawo likufunafuna moyo wanga,+
Ndipo sanakuikeni patsogolo pawo.+
15 Koma inu Yehova, ndinu Mulungu wachifundo ndi wachisomo,+
Wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.+