Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide.
14 Wopusa amanena mumtima mwake kuti:
“Kulibe Yehova.”+
Anthu oterewa amachita zoipa,+ ndipo amachita zinthu zonyansa.
Palibe amene akuchita zabwino.+
2 Koma kuchokera kumwamba, Yehova wayang’ana ana a anthu padziko lapansi,+
Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, aliyense amene akufunafuna Yehova.+
3 Onse apatuka,+ ndipo onsewo ndi achinyengo.+
Palibe aliyense amene akuchita zabwino,+
Palibiretu ndi mmodzi yemwe.+
4 Kodi palibe aliyense wozindikira mwa anthu ochita zopweteka anzawowa,+
Amene akudya anthu anga ngati chakudya?+
Iwo sanaitane pa Yehova.+