Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda.
133 Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri
Abale akakhala pamodzi mogwirizana!+
2 Zili ngati mafuta abwino amene athiridwa pamutu,+
Amene akutsikira kundevu,
Ndevu za Aroni,+
Amenenso akuyenderera mpaka m’khosi la zovala zake.+
3 Zili ngati mame+ a ku Herimoni,+
Amene akutsikira pamapiri a ku Ziyoni.+
Pakuti Yehova analamula dalitso kukhala kumeneko,+
Walamulanso kuti kukhale moyo mpaka kalekale.+