Masalimo
ג [Giʹmel]
2 Ana ake adzakhala amphamvu padziko lapansi.+
ד [Daʹleth]
Ndipo m’badwo wa anthu olungama udzadalitsidwa.+
ה [Heʼ]
3 Zinthu zamtengo wapatali ndiponso chuma zili m’nyumba yake,+
ו [Waw]
Ndipo chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+
ז [Zaʹyin]
4 Waunika mu mdima kuti anthu owongoka mtima aone kuwala.+
ח [Chehth]
Iye ndi wachisomo, wachifundo ndi wolungama.+
ט [Tehth]
5 Munthu wachisomo+ komanso wokongoza ena zinthu ndi wabwino.+
י [Yohdh]
Amachita zinthu mwachilungamo.+
כ [Kaph]
6 Ndithudi munthu wotero sadzagwedezeka ngakhale pang’ono.+
ל [Laʹmedh]
Wolungama adzakumbukiridwa mpaka kalekale.+
מ [Mem]
ס [Saʹmekh]
8 Mtima wake sungagwedezeke,+ ndipo sadzachita mantha,+
ע [ʽAʹyin]
Pamapeto pake adzayang’ana adani ake atagonjetsedwa.+
פ [Peʼ]
9 Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu aumphawi.+
צ [Tsa·dhehʹ]
Chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+
ר [Rehsh]
10 Woipa adzaona zimenezi ndipo adzasautsika.+
ש [Shin]
Adzakukuta mano ndi kusungunuka.+
ת [Taw]
Chikhumbo cha anthu oipa chidzatha.+