Masalimo Nyimbo ya Asafu. 82 Mulungu waima pakati pa msonkhano wake,+Ndipo akuweruza pakati pa milungu kuti:+ 2 “Kodi mudzaweruza mopanda chilungamo,+Ndi kukondera anthu oipa kufikira liti?+ [Seʹlah.] 3 Chitirani chilungamo anthu onyozeka ndi ana amasiye.*+Chitirani chilungamo anthu osautsika ndi osauka.+ 4 Pulumutsani munthu wonyozeka ndi wosauka.+Alanditseni m’manja mwa anthu oipa.”+ 5 Milunguyo siikudziwa kanthu ndipo siikuzindikira.+Ikuyendayenda mu mdima,+Ndipo maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.+ 6 “Ine ndanena kuti, ‘Inu ndinu milungu,+Ndipo nonsenu ndinu ana a Wam’mwambamwamba.+ 7 Ndithudi, mudzafa mmene anthu onse amafera.+Ndipo mudzagwa mmene kalonga aliyense amagwera!’”+ 8 Nyamukani inu Mulungu, weruzani dziko lapansi.+Pakuti inu nokha muyenera kutenga mitundu yonse kukhala yanu.+