Masalimo
Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.+
Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
4 Ndikumbukireni inu Yehova, ndipo ndisonyezeni kukoma mtima kumene mumasonyeza anthu anu.+
Ndisamalireni ndi kundipulumutsa,+
5 Kuti ndione ubwino umene mumapereka kwa osankhidwa anu,+
Kuti ndikondwere pamene mtundu wanu ukukondwera,+
Ndiponso kuti ndinyadire pamodzi ndi cholowa chanu.+
7 Makolo athu ku Iguputo,
Sanasonyeze kuzindikira kulikonse ntchito zanu zodabwitsa.+
Sanakumbukire kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha,+
Koma anapanduka panyanja, pafupi ndi Nyanja Yofiira.+
9 Choncho anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo pang’onopang’ono nyanjayo inauma.+
Pamenepo anawayendetsa kudutsa pakati pa madzi akuya ngati akuwayendetsa m’chipululu.+
10 Chotero anawapulumutsa m’manja mwa wodana nawo,+
Ndipo anawawombola m’manja mwa mdani.+
15 Mulungu anawapatsa zimene anali kupempha,+
Ndipo anawagwetsera matenda a kaliwondewonde pakati pawo.+
19 Iwo anapanganso mwana wa ng’ombe ku Horebe,+
Ndipo anaweramira chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+
20 Choncho anasinthanitsa ulemerero wanga+
Ndi chifaniziro cha ng’ombe yamphongo yodya udzu.+
21 Iwo anaiwala Mulungu, Mpulumutsi wawo,+
Amene anachita zinthu zazikulu ku Iguputo,+
22 Amene anachita zodabwitsa m’dziko la Hamu,+
Amene anachita zochititsa mantha pa Nyanja Yofiira.+
23 Iye anangotsala pang’ono kulamula kuti awawononge,+
Koma Mose wosankhidwa wake,
Anaima pamalo ogumuka pamaso pa Mulungu,+
Ndi kubweza mkwiyo wake kuti usawawononge.+
26 Choncho Mulungu anawalumbirira atakweza dzanja lake,+
Kuti adzawapha m’chipululu,+
27 Ndiponso kuti adzachititsa ana awo kuphedwa ndi mitundu ina,+
Ndi kuti adzawamwaza m’mayiko osiyanasiyana.+
32 Kuwonjezera pamenepo, iwo anaputa mkwiyo pa madzi a ku Meriba,+
Moti Mose sizinamuyendere bwino chifukwa cha anthu amenewa.+
38 Choncho anali kukhetsa magazi a anthu osalakwa,+
Magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi,
Amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani.+
Ndipo dzikolo linaipa ndi magazi amene iwo anakhetsa.+
41 Mobwerezabwereza anali kuwapereka m’manja mwa anthu a mitundu ina,+
Kuti anthu odana nawo awalamulire,+
42 Ndi kuti adani awowo awapondereze,
Komanso kuti awagonjetse.+
43 Nthawi zambiri anali kuwalanditsa,+
Koma iwo anali kumupandukira chifukwa sanali kumumvera,+
Ndipo anali kuwatsitsa chifukwa cha zolakwa zawo.+
45 Zikatero anali kukumbukira pangano limene anachita ndi iwo,+
Ndipo anali kuwamvera chisoni chifukwa cha kuchuluka kwa kukoma mtima kwake kosatha.+