17 Kenako Mulungu anauza Adamu kuti: “Popeza wamvera mawu a mkazi wako, ndipo wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti,+ ‘Usadzadye zipatso zake,’ nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi.+ Udzavutika kulima nthakayo masiku onse a moyo wako+ kuti upeze chakudya.